On air

Now: Halaal |Next 17:00: Mwaweruka Bwanji

--:--CAT
Watch live

News

FAM Yimaliza Kukonza Ndondomeko Ya Zachuma

Bungwe loyendetsa mpira wa miyendo m’dziko muno la Football Association of Malawi (FAM) lamaliza zokambirana ndi mabungwe omwe ali pansi pake ndi anthu ena okhudzidwa ndi mpira pa ndondomeko ya chuma ya chaka cha 2027, pofuna kupititsa patsogolo masewerowa m’magawo zosiyanasiyana.

Poyankhula pa msonkhano womaliza wa zokambiranazi womwe wachitikira mu mzinda wa Lilongwe, mtsogoleri wa FAM, Fleetwood Haiya, wati ndondomeko ya zachuma yomwe bungweli likukonzekera ndi yokwana K21.8 biliyoni.

A Haiya ati ndalama zambiri zikuyembekezeka kuchokera kwa othandizira komanso njira zina zopezera ndalama.

Malinga ndi a Haiya, zokambiranazi zathandiza kuonetsetsa kuti ndondomekoyi ikugwirizana ndi ntchito zofunika pa chitukuko cha mpira.

A haiya ati ndondomeko ikukonzekera kugwiritsa ntchito K21.2 biliyoni, pomwe ndalama zokwana K594 miliyoni zikuyembekezeka kutsala ngati ndalama zosungidwira ntchito zadzidzidzi.

Ndondomekoyi ikaperekedwa ku msonkhano waukulu wa FAM mwezi wamawa kuti ukavomereze. 

Bungwe la National Youth Football Association ndi lomwe likuyembekezeka kulandira ndalama zambiri zokwana K2.8 biliyoni.

Mtsogoleri wa bungweli, Tiyenkhu Chavula, wati nthawi yakwana yoti pakhale ndalama zambiri zolimbikitsira chitukuko cha mpira wa achinyamata, ati poti ndi njira yofunika kwambiri yotukulira masewerowa m’dziko muno.

Keep reading

More news

All news →
Advertise on TV Islam

Grow your brand. Reach your audience.

Advertise on TV Islam: on television across Malawi, on Facebook Live and on YouTube.

Call+265 999 345 786
+265 888 345 786
Emailstation.manager@tvislam.mw
VisitGlobal House, Second Floor
Raynor Avenue, Limbe
WriteP.O. Box 5866
Limbe, Malawi